Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 21:11-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo za nyumba ya mfumu ya Yuda, tamvani mau a Yehova:

12. Nyumba ya Davide iwe, Yehova atero, Cita ciweruzo m'mawa, ndi kumlanditsa amene afunkhidwa m'dzanja la wosautsa, kungaturuke kupsa mtima kwanga ngati moto, ndi kutentha kosazimika, cifukwa ca nchito zanu zoipa,

13. Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'cigwa, ndi pa thanthwe la m'cidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?

14. Ndipo ndidzakulangani inu monga mwa cipatso ca nchito zanu, ati Yehova; ndipo ndidzayatsa moto m'nkhalango mwace, ndipo udzatha zonse zomzungulira iye.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 21