Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 2:6-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Osati, Ali kuti Yehova amene anatikweza kucokera ku dziko la Aigupto, natitsogolera m'cipululu, m'dziko loti se ndi la maenje, m'dziko la cirala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitamo anthu, losamangamo anthu?

7. Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zace, ndi zabwino zace; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa colandira canga conyansa.

8. Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula.

9. Cifukwa cace ndidzatsutsananso nanu, ati Yehova, ndi ana a ana anu ndidzatsutsana nao.

10. Pakuti pitani ku zisumbu za Kitimu nimuone; tumizani ku Kedara nimulingalire bwino; nimuone ngati cinalipo cotere.

11. Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siiri milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi cosapindula.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 2