Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 2:22-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu.

23. Bwanji uti, Sindinaipitsidwa, sindinatsata Abaala? Ona njira yako m'cigwa, dziwa cimene wacicita; ndiwe ngamila yothamanga yoyenda m'njira zace;

24. mbidzi yozolowera m'cipululu, yopumira mphepo pakufuna pace; pokomana nayo ndani adzaibweza? onse amene aifuna sadzadzilemetsa; adzaipeza m'mwezi wace.

25. Kaniza phazi lako lisakhale losabvala nsapato, ndi m'mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe ciyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao.

26. Monga mbala iri ndi manyazi pamene igwidwa, comweco nyumba ya Israyeli iri ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akuru ao, ansembe ao, ndi aneneri ao;

27. amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kubvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.

28. Koma iri kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kubvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kucuruka kwa midzi yako, Yuda iwe.

29. Cifukwa canji mudzatsutsana ndi Ine nonse? mwandilakwira Ine, ati Yehova.

30. Ndapanda ana anu mwacabe; sanamvera kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.

31. Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israyeli cipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Cifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?

32. Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zace, kapena mkwatibwi zobvala zace? koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.

33. Kodi sukonzadi njira yako kufunafuna cilakolako? cifukwa cace waphunzitsa akazi oipa njira zako.

34. Ndiponso m'nsaru zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osacimwa; sunawapeza pakuboola, koma ponsepo.

35. Koma unati, Ndiri wosacimwa ndithu; mkwiyo wace wacoka pa ine. Taona, ndidzakuweruza iwe, cifukwa uti, Sindinacimwa.

36. Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? udzacitanso manyazi ndi Aigupto monga unacita manyazi ndi Asuri.

37. Koma udzaturuka kwa iyenso, manja ako pamtu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 2