Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 2:20-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Pakuti kale lomwe ndinatyola gori lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitari, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kucita dama.

21. Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pace, ya mpesa wacilendo?

22. Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu.

23. Bwanji uti, Sindinaipitsidwa, sindinatsata Abaala? Ona njira yako m'cigwa, dziwa cimene wacicita; ndiwe ngamila yothamanga yoyenda m'njira zace;

24. mbidzi yozolowera m'cipululu, yopumira mphepo pakufuna pace; pokomana nayo ndani adzaibweza? onse amene aifuna sadzadzilemetsa; adzaipeza m'mwezi wace.

25. Kaniza phazi lako lisakhale losabvala nsapato, ndi m'mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe ciyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao.

26. Monga mbala iri ndi manyazi pamene igwidwa, comweco nyumba ya Israyeli iri ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akuru ao, ansembe ao, ndi aneneri ao;

27. amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kubvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.

28. Koma iri kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kubvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kucuruka kwa midzi yako, Yuda iwe.

29. Cifukwa canji mudzatsutsana ndi Ine nonse? mwandilakwira Ine, ati Yehova.

30. Ndapanda ana anu mwacabe; sanamvera kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 2