Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 2:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Muzizwe pamenepo, miyamba inu, muope kwambiri, mukhale ouma, ati Yehova.

13. Pakuti anthu anga anacita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong'aluka, zosakhalamo madzi.

14. Kodi Israyeli ndi mtumiki? kodi ndiye kapolo wobadwa m'nyumba? afunkhidwa bwanji?

15. Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lace, midzi yace yatenthedwa, mulibenso wokhalamo.

16. Ananso a Nofi ndi a Tahapanesi, anaswa pakati pamtu pako.

17. Kodi sunadzicitira ici iwe wekha popeza unasiya Yehova Mulungu wako, pamene anatsogolera iwe panjira?

18. Tsopano uli naco ciani m'njira ya ku Aigupto, kumwa madzi a Sihori? uli naco ciani m'njira ya ku Asuri, kumwa madzi a m'Nyanja?

19. Coipa cako cidzai kulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ici ndi coipa ndi cowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Yehova Mulungu wa makamu.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 2