1. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, nati,
2. Pita nupfuule n'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, cikondi ca matomedwe ako; muja unanditsata m'cipululu m'dziko losabzya lamo.
3. Israyeli anali wopatulikira Yehova, zipatso zoundukula za zopindula zace; onse amene adzamudya iye adzayesedwa oparamula; coipa cidzawagwera, ati Yehova.