Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 18:13-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Cifukwa cace atero Yehova; Funsanitu m'mitundu, ndani wamva zotero; namwali wa Israyeli wacita cinthu coopsetsa kwambiri.

14. Kodi matalala a Lebano adzalephera pa mwala wa m'munda? kodi adzaphwa madzi ozizira otsika kutari?

15. Pakun anthu anga andiiwala Ine, afukizira zopanda pace; apunthwitsa iwo m'njira zao, m'njira zakale kuti ayende m'njira za m'mbali, m'njira yosatundumuka;

16. kuti aliyese dziko lao likhale lodabwitsa, ndi: kutsonya citsonyere; yense wakupitapo adzadabwa, ndi kupukusa mutu wace.

17. Ndidzamwazamwaza iwo monga ndi mphepo ya kum'mawa pamaso pa adani; ndidzayang'anira pamsana pao, si nkhope yao, tsiku la tsoka lao.

18. Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya comcitira coipa; pakuti cilamulo sicidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ace ali onse.

19. Mundimvere ine, Yehova, mumve mau a iwo akulimbana ndi ine.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 18