Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 17:22-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. musaturutse katundu m'nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire nchito iri onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu;

23. koma sanamvera, sanachera khutu lao, koma anaumitsa khosi lao, kuti asamve, asalandire langizo.

24. Ndipo padzakhala, ngati mu ndimveretsa Ine, ati Yehova, kuti musalowetse katundu pa zipata za mudzi uwu tsiku la Sabata, koma mupatule tsiku la Sabata, osagwira nchito m'menemo;

25. pamenepo padzalowa pa zipata za mudzi uwu mafumu ndi akuru okhala pa mpando wacifumu wa Davide, okwera pa magareta ndi akavalo, iwo, ndi akuru ao, anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; ndipo mudzi uwu udzakhala ku nthawi zamuyaya.

26. Ndipo adzacokera ku midzi ya Yuda, ndi ku malo akuzungulira Yerusalemu, ndi ku dziko la Benjamini, ndi kucidikha, ndi kumapiri, ndi ku Mwela, ndi kudza nazo nsembe zopsereza, ndi nsembe zophera, ndi nsembe zaufa, ndi zonunkhira, ndi kudza nazo zamiyamikiro, ku nyumba ya Yehova.

27. Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m'zipata zacezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 17