Pamenepo uziti kwa iwo, Cifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu yina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga cilamulo canga;