Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 15:15-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang'anire ine, mundibwezere cilango pa ondisautsa ine; musandicotse m'cipiriro canu; dziwani kuti cifukwa ca Inu ndanyozedwa.

16. Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine cikondwero ndi cisangalalo ca mtima wanga; pakuti ndachedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.

17. Sindinakhala m'msonkhano wa iwo amene asekera-sekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha cifukwa ca dzanja lanu; pakuti mwandidzaza ndi mkwiyo.

18. Kupweteka kwanga kuti cipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?

19. Cifukwa cace atero Yehova, Ukabwerera pamenepo ndidzakubwezanso, kuti uime pamaso panga; ndipo ukasiyanitsa ca mtengo wace ndi conyansa, udzakhala ngati m'kamwa mwanga; ndipo adzabwerera kwa iwe, koma sudzabwerera kwa iwo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 15