Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 14:19-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Kodi mwakanadi Yuda? kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? bwanji mwatipanda ife, ndipo tiribe kucira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakucira, ndipo taonani mantha!

20. Tibvomereza, Yehova, cisalungamo cathu, ndi coipa ca makolo athu; pakuti takucimwirani Inu.

21. Musatinyoze ife, cifukwa ca dzina lanu; musanyazitse mpando wacifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife.

22. Mwa zacabe za mitundu ya anthu ziripo kodi, zimene zingathe kubvumbitsa mvula? Kodi si ndinu, Yehova, Mulungu wathu? ndipo tidzakudikirani Inu; pakuti munalenga zonse zimenezi.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 14