Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 11:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo midzi ya Yuda ndi okhala m'Yerusalemu adzapita nadzapfuulira kwa milungu imene anaifukizira; koma siidzawapulumutsa konse nthawi ya nsautso yao.

13. Pakuti milungu yako ilingana ndi kucuruka kwa midzi yako, iwe Yuda; ndi maguwa a nsembe amene mwautsira camanyazi, alingana ndi kucuruka kwa miseu ya Yerusalemu, ndiwo maguwa akufukizirapo Baala.

14. Cifukwa cace usawapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu, kapena pemphero, pakuti sindidzamva iwo nthawi imene andipfuulira Ine m'kusaukakwao.

15. Wokondedwa wanga afunanji m'nyumba mwanga, popeza wacita coipa ndi ambiri, ndipo thupi lopatulika lakucokera iwe? pamene ucita coipa ukondwera naco.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 11