Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 1:6-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! taonani, sindithai kunena pakuti ndiri mwana.

7. Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena conse cimene ndidzakuuza.

8. Usaope nkhope zao; cifukwa Ine ndiri ndi iwe kuti ndikulanditse iwe, ati Yehova.

9. Ndipo Yehova anaturutsa dzanja lace, na'khudza pakamwa panga; nati Yehova kwa ine, Taona ndaika mau anga m'kamwa mwako;

10. penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uononge, ugwetse; umange, ubzyale.

11. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Yeremiya, uona ciani? Ndipo ndinati, Ine ndiona ntyole ya katungurume.

12. Ndipo Yehova anati kwa ine, Waona bwino pakuti Ine ndidzadikira mau anga kuwacita.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 1