Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Rute 2:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Nati Boazi kwa mnyamata wace woyang'anira ocekawo, Mkazi uyu ngwa yani?

6. Ndipo mnyamata woyang'anira ocekawo anayankha nati, Ndiye mkazi Mmoabuyo anabwera ndi Naomi ku dziko la Moabu;

7. ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ocekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo.

8. Pamenepo Boazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakunkha m'munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno.

9. Maso ako akhale pa munda acekawo, ndi kuwatsata; kodi sindinawauza anyamata asakukhudze? Ndipo ukamva ludzu, muka kumitsuko, ukamweko otunga anyamatawo,

10. Potero anagwa nkhope yace pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima cifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?

11. Ndipo Boazi anayankha nanena naye, Anandifotokozera bwino zonse unacitira mpongozi wako atafa mwamuna wako; ndi kuti wasiya atate wako ndi mako, ndi dziko lobadwirako iwe, ndi kudza kwa anthu osawadziwa iwe kale.

12. Yehova akubwezere nchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israyeli, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ace.

Werengani mutu wathunthu Rute 2