Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Rute 2:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Naomi anali nave mbale wa mwamuna wace, ndiye munthu mwini cuma cambiri wa banja la Elimeleki; dzina lace ndiye Boazi.

2. Nati Rute Mmoabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha is ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomeramtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.

3. Namuka iye, nakatola khunkha m'munda namatsata ocekawo; ndipo kudangotero naye kuti deralo la munda linali la Boazi, ndiye wa banja la Elimeleki.

4. Ndipo taona, Boazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa oceka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.

5. Nati Boazi kwa mnyamata wace woyang'anira ocekawo, Mkazi uyu ngwa yani?

6. Ndipo mnyamata woyang'anira ocekawo anayankha nati, Ndiye mkazi Mmoabuyo anabwera ndi Naomi ku dziko la Moabu;

7. ndipo anati, Undilole, ndikunkhe ndiole pakati pa mitolo potsata ocekawo; nadza iye nakhalakhala kuyambira m'mawa mpaka tsopano; koma m'nyumba samakhalitsamo.

8. Pamenepo Boazi ananena ndi Rute, Ulikumva, mwana wanga? Usakakunkha m'munda mwina, kapena kupitirira pano, koma uumirire adzakazi anga mommuno.

Werengani mutu wathunthu Rute 2