Nati Rute Mmoabu kwa Naomi, Mundilole ndimuke kumunda, ndikatole khunkha is ngala za tirigu, kumtsata iye amene adzandikomeramtima. Nanena naye, Muka, mwana wanga.