Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 9:7-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu pa phiri la Gerizimu, nakweza mau ace, napfuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ace a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu.

8. Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu; niti kwa mtengo waazitona, Ukhale iwe mfumu yathu.

9. Koma mtengo waazitona unati kwa iwo, Ngati ndidzasiya kunona kwanga kumene alemekeza nako Mulungu ndi anthu kukalenga pa mitengo?

10. Pamenepo mitengo inati kwa mkuyu. Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.

11. Koma mkuyu unanena nao, Ngati ndidzasiya kuzuna kwanga, ndi zipatso zanga zokoma kukalenga pa mitengo?

12. Pamenepo mitengo inati kwa mpesa, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.

13. Koma mpesa unanena nao, Ngati ndidzasiya vinyo wanga wakusekeretsa Mulungu ndi anthu, kukalenga pa mitengo?

14. Pamenepo mitengo yonse inati kwa nkandankhuku, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.

15. Ndipo nkandankhuku unati kwa mitengo, Mukandidzoza mfumu yanu moonadi, tiyeni, thawirani ku mthunzi wanga; mukapanda kutero uturuke mota m'nkandankhuku ndi kunyeketsa mikungudza ya Lebano.

16. Ndipo tsopano, ngati mwacita moona ndi mwangwiro pakulonga Abimeleki ufumu, ngatinso mwamcitira cokoma Yerubaala ndi nyumba yace, ndi kumcitira monga anayenera manja ace;

17. pakuti atate wanga anakugwirirani nkhondo, nataya moyo wace, nakupulumutsani m'dzanja la Amidyani;

Werengani mutu wathunthu Oweruza 9