Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 9:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo tsopano, ngati mwacita moona ndi mwangwiro pakulonga Abimeleki ufumu, ngatinso mwamcitira cokoma Yerubaala ndi nyumba yace, ndi kumcitira monga anayenera manja ace;

17. pakuti atate wanga anakugwirirani nkhondo, nataya moyo wace, nakupulumutsani m'dzanja la Amidyani;

18. koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ace, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wace, akhale mfumu ya pa eni ace a ku Sekemu, cifukwa ali mbale wanu;

19. ngati tsono mwacitira Yerubaala ndi nyumba yace zoona ndi zangwiro lero lino, kondwerani naye Abimeleki, nayenso akondwere nanu;

20. koma ngati simunatero, uturuke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ace a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nuturuke mota kwa eni ace a ku Sekemu, ndi ku nyumba yace ya Milo, nunyeketse Abimeleki.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 9