Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 4:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo Ambuye anaononga Sisera, ndi magareta onse ndi gulu lankhondo lonse, adi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagareta nathawa coyenda pansi.

16. Koma Baraki anatsata magareta ndi gululo mpaka Haroseti wa amitundu; ndi gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa, sanatsala munthu ndi mmodzi yense.

17. Koma Sisera anathawira coyenda pansi ku hema wa Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni; pakuti panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori, ndi nyumba ya Heberi Mkeni.

18. Ndipo Yaeli anaturuka kukomana ndi Sisera, nanena naye, Pambuka, mbuye wanga, pambukira kwa ine kuno; usaope. Ndipo anapambukira kwa iye kulowa m'hema, nampfunda ndi cimbwi.

19. Pamenepo ananena naye, Ndipatsetu madzi pang'ono ndimwe; popeza ndine waludzu. Ndipo anatsegula thumba la mkaka, nampatsa amwe, nampfunda.

20. Ndipo Sisera ananena naye, Taima pakhomo pa hema, ndipo kudzali, akadza munthu, akakufunsa akati, Pali munthu pano kodi? Uziti, Palibe.

21. Pamenepo Yaeli mkazi wa Heberi anatenga ciciri ca hema, natenga nyundo m'dzanja lace namdzera monyang'ama, nakhomera ciciri cilowe m'litsipa mwace; nicinapyoza kulowa m'nthaka; popeza anali m'tulo tofa nato ndi kulema; nafa.

22. Ndipo taonani, pomlondola Sisera Barakiyo, Yaeli anaturuka kukomana naye, Dati kwa iye, Idza kuno, ndidzakuonetsa munthu umfunayo, Potero anamdzera, ndipo taonani, Sisera wagwa, wafa, ndi ciciri m'litsipa mwace.

23. Momwemo Mulungu anagonjetsa tsiku lija Yabini mfumu ya Kanani pamaso pa ana a Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 4