Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 4:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ana a Israyeli anaonjeza kucita coipa pamaso pa Yehova, atafa Ehudi.

2. Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wocita ufumu ku Hazori; kazembe wace wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu.

3. Ndipo ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova; pakuti anali nao magareta acitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israyeli kolimba zaka makumi awiri.

4. Ndipo Debora, mneneri wamkazi, ndiye mkazi wace wa Lapidoti, anaweruza Israyeli nyengo ija,

5. Ndipo anakhala patsinde pa mgwalangwa wa Debora pakati pa Rama ndi Beteli ku mapiri a Efraimu; ndi ana a Israyeli anakwera kwa iye awaweruze.

6. Ndipo anatuma, naitana Baraki mwana wa Abinoamu, acoke m'Kedesi-Nafitali; nanena naye, Kodi Yehova Mulungu wa Israyeli sanalamulira ndi kuti, Muka, nuluniike ku phiri la Tabori, nuwatenge, apite nawe anthu zikwi khumi a ana a Nafitali ndi ana a Zebuloni?

7. Ndipo ndidzamkoka Sisera, kazembe wa nkhondo ya Yabini, akudzere ku mtsinje wa Kisoni, ndi magareta ace, ndi aunyinji ace; ndipo ndidzampereka m'dzanja lako.

8. Ndipo Baraki anati kwa iye, Ukamuka nane, ndidzamuka; ukapanda kumuka nane, sindimuka.

9. Nati iye, Kumuka ndidzamuka nawe, koma ulendo umukawo, sudzacita nao ulemu; pakuti: Yehova adzagulitsa Sisera m'dzanja la mkazi, Motero Debora anauka namuka ndi Baraki ku Kedesi.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 4