Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 3:15-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Koma pamene ana a Israyeli anapfuula kwa Yehova, Yehova anawaukitsira mpulumutsi, Ehudi mwana wa Gera, Mbenjamini, munthu wamanzere, ndipo ana a Israyeli anatumiza mtulo m'dzanja lace Ikwa Egiloni mfumu ya Moabu.

16. Ndipo Ehudi anadzisulira lupanga lakuthwa konse konse utali wace mkono; nalimangirira pansi pa zobvala zace pa ncafu ya kulamanja.

17. Ndipo anapereka mtulo kwa Egiloni, mfumu ya Moabu; koma Egiloni ndiye munthu wonenepa ndithu.

18. Ndipo atatha kupereka mtulowo, anauza anthu onyamula mtulo acoke.

19. Koma iye mwini anabwerera pa mafano osema ali ku Giligala, nati, Ndiri nao mau acinsinsi kwa inu, mfumu. Nati iye, Khalani cete. Ndipo anaturuka onse akuimapo.

20. Ndipo Ehudi anamdzera alikukhala pa yekha m'cipinda cosanja copitidwa mphepo, Nati Ehudi, Ndiri nao mau a Mulungu akukuuzani. Nauka iye pa mpando wace.

21. Ndipo Ehudi anaturutsa dzanja lace lamanzere nagwira lupanga ku ncafu ya kulamanja nampyoza m'mimba mwace;

22. ndi cigumbu cace cinalowa kutsata mpeni wace; ndi mafuta anaphimba mpeniwo, pakuti sanasolola lupanga m'mimba mwace; nilituruka kumbuyo.

23. Pamenepo Ehudi anaturuka kukhonde namtsekera pamakomo pa cipinda cosanja nafungulira.

24. Ndipo ataturuka iye, anadza aka polo ace; napenya, ndipo taonani pamakomo pa cipinda cosanja mpofungulira; nati iwo, Angophimba mapazi m'cipinda cace cosanja copitidwa mphepo.

25. Ndipo analindirira mpaka anacita manyazi; koma taonani, sanatsegula pamakomo pa cipinda cosanja. Pamenepo anatenga mfungulo natsegula; ndipo taonani, mbuye wao wagwa pansi, wafa.

26. Ndipo Ehudi anapulumuka pakucedwa iwo, napitirira pa mafano osema, napulumuka kufikira Seira.

27. Ndipo kunali, pakufika iye anaomba lipenga ku mapiri a Efraimu; ndi ana a Israyeli anatsika naye kucokera kumapiri, nawatsogolera iye.

28. Ndipo ananena nao, Nditsateni ine, pakuti Yehova wapereka adani anu Amoabu m'manja mwanu. Ndipo anatsika ndi kumtsata, natsekereza Amoabu madooko a Yordano, osalola mmodzi aoloke.

29. Ndipo anakantha Amoabu nyengo ija anthu zikwi khumi, onsewa anthu amoyo, ndi ngwazi; ndipo sanapulumuka ndi mmodzi yense.

30. Motero anagonjetsa Moabu tsiku lija pansi pa dzanja la Israyeli. Ndipo dziko linapumulazaka makumi asanu ndi atatu.

31. Atapita iye kunali Samagara, mwana wa Anati amene anakantha Afilisti mazana asanu ndi limodzi ndi mtoso wa ng'ombe; nayenso anapulumutsa Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 3