Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 21:12-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo anapeza mwa anthu a Yabesi-gileadi anamwali mazana anai osadziwa mwamuna mogona naye; nabwera nao kumisasa ku Silo, ndiwo a m'dziko la Kanani.

13. Ndipo msonkhano wonse unatumiza mau kwa ana a Benjamini okhala m'thanthwe la Rimoni, nawalalikira mtendere.

14. Nakwera Abenjamini nthawi ija, ndipo anawapatsa akazi amene anawasunga amoyo mwa akazi a Yabesi-gileadi; koma sanawafikira.

15. Ndipo anthu anamva cifundo pa Benjamini, pakuti Yehova adang'amba mapfuko a Israyeli.

16. Pamenepo akuru a msonkhano anati, Tidzatani, kuwafunira akazi otsalawo, popeza akazi anatha psiti m'Benjamini?

17. Nati iwo, Pakhale colowa ca iwo opulumuka a Benjamini, lingafafanizidwe pfuko m'Israyeli.

18. Koma sitikhoza ife kuwapatsa ana athu akazi akhale akazi ao; pakuti ana a Israyeli adalumbira ndi kuti, Atembereredwe wakupatsa Abenjamini mkazi.

19. Natiiwo, Taonani, pali madyerero a Yehova caka ndi caka ku Silo, ndiko kumpoto kwa Beteli, kum'mawa kwa mseu wokwera kucokera ku Beteli kumka ku Sekemu, ndi kumwela kwa Lebona.

20. Ndipo analamulira ana a Benjamini ndi kuti, Mukani, mulalire m'minda yamphesa;

21. nimuyang'ane, ndipo taonani, ataturuka ana akazi a Silo kubvinabvina, pamenepo muturuke m'minda yamphesa ndi kudzigwirira yense mkazi wace mwa ana akazi a Silo, ndi kumuka naye ku dziko la Benjamini.

22. Ndipo kudzali, akatifikira atate ao kapena alongo ao kunena nafe mlandu, tidzanena nao, Mutipatse awa, pakuti sitinawatengera yense mkazi wace kunkhondo; pakuti inunso simunawaninkha awa; mukadatero mukadaparamula tsopano.

23. Nacita cotere ana a Benjamini, nadzitengera akazi monga mwa kuwerenga kwao, a obvina aja, amene anawatenga mwacifwamba; namuka iwo nabwerera ku colowa cao, namanga midzi, nakhalamo.

24. Ndipo ana a Israyeli anacokako nthawi ija yense kumka ku pfuko lace, ndi banja lace, naturukako yense kumka ku colowa cace.

25. Panalibe mfumu m'Israyeli masiku aja; a yense anacita comkomera pamaso pace.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 21