Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 18:7-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Pamenepo amuna asanuwa anacoka, nafika ku Laisi; naona anthu anali m'mwemo, kuti anakhalaokhazikika mtima, monga anakhala Asidoni, odekha ndi osatekeseka; popeza m'dzikomo munalibe mwini bwalo wakudtitsa manyazi m'cinthu ciri conse; nasiyana kutali ndi Asidoni, ndipo analibe kanthu ndi munthu ali yense.

8. Ndipo asanuwo anafikanso kwa abale ao ku Zora ndi Esitaoli; ndi abale ao ananena nao, Mutani inu?

9. Nati iwo, Taukani, tiwakwerere; pakuti tapenya dziko, ndipo taonani, ndilo lokoma ndithu; ndi inu muli cete kodi? musamacita ulesi kumuka ndi kulowa kulandira dzikolo,

10. Pomuka inu mudzafikira anthu okhazikika mtima ndi dziko ladtando; pakuti Mulungu walipereka m'dzanja lanu; pamenepo mposasowa kanthu kali konse kali pa dziko lapansi.

11. Pamenepo amuna mazana asanu ndi limodzi, omangira zida za nkhondo m'cuuno, anaphumulako a banja la a Dani, anacokera ku Zora, ndi ku Esitaoli.

12. Nakwera namanga misasa m'Kiriyati-yearimu, m'Yuda; cifukwa cace anacha dzina lace la malowo cigono ca Dani, mpaka lero; taona, ali m'tseri mwa Kiriyatiyearimu.

13. Ndipo anapiririra komweko kumka ku mapiri a Efraimu, nadza ku nyumba ya Mika.

14. Pamenepo anayankha amuna asanu anamukawo kukazonda dziko la Laisi, nanena ndi abale ao, Kodi mudziwa kuti m'nyumba izi muli cobvala ca wansembe, ndi timafano ndi fano losema, ndi fano loyenga? Ndipo tsopano dziwani coyenera inu kucita.

15. Napambuka iwo kumkako, nafika ku nyumba ya mnyamata Mleviyo, ndiyo nyumba ya Mika, namfunsa ngati ali bwanji.

16. Ndipo amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida zao za nkhondo m'cuuno, ndiwo a ana a-Dani, analikuima polowera pa cipata;

17. koma amuna asanu omukawo kukazonda dziko anakwera nalowako, natenga fano losema, ndi cobvala ca wansembe ndi timafano, ndi fano loyenga; ndi wansembe anaima polowera pa cipata pamodzi ndi amuna mazana asanu ndi limodzi omangira zida za nkhondo m'cuuno.

18. Atalowa iwo m'nyumba ya Mika, natengako fane losema, cobvala ca wansembe, ndi timafano, ndi fano loyenga, wansembeyo ananena nao, Mucitanji?

19. Ndipo ananena naye, Khala cete, tseka pakamwa pako, numuke nafe, nutikhalire atate ndi wansembe wathu; cikukomera nciti, kukhala wansembe wa nyumba ya munthu mmodzi, kapena kukhala wansembe wa pfuko ndi banja m'Israyeli?

20. Nukondwera mtima wa wansembeyo, natenga iye cobvala ca wansembe, ndi timafano ndi fano losema, nalowa pakati pa anthu.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 18