Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 18:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Masiku ajawo panalibe mfumu m'Israyeli; masiku ajanso pfuko la Adani anadzifunira colowa cakukhalako; pakuti kufikira tsiku lija sicinawagwera colowa cao pakati pa mapfuko a Israyeli.

2. Ndipo ana a Dani anatuma a banja lao amuna asanu a mwa iwo onse, anthu olimba mtima, a ku Zora, ndi a ku Esitaoli, a kuzonda dziko ndi kufunafunamo; nanena nao, Mukani, mufunefune m'dziko. Nafika iwo ku mapiri a Efraimu ku nyumba ya Mika, nagona komweko,

3. Pokhala iwo m'nyumba ya Mika, anazindikira mau a mnyamata Mleviyo, napambukirako, nanena naye, Anadza nawe kuno ndani? ucitanji muno? ukhala naco ciani kuno?

4. Ndipo ananena nao, Mika anandicitira cakuti cakuti, napangana nane za nchito, ndipo ndikhala wansembe wace.

5. Pamenepo ananena naye, Utifunsire kwa Mulungu, kuti tidziwe ngati ulendo wathu timukawo udzakoma.

6. Nanena nao wansembeyo, Mukani mumtendere, ulendo wanu muyendawo uli pamaso pa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 18