Masiku ajawo panalibe mfumu m'Israyeli; masiku ajanso pfuko la Adani anadzifunira colowa cakukhalako; pakuti kufikira tsiku lija sicinawagwera colowa cao pakati pa mapfuko a Israyeli.