Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 16:24-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo pakumuona anthu analemekeza mulungu wao, pakuti anati, Mulungu wathu wapereka m'dzanja lathu mdani wathu, ndiye wakupasula dziko lathu, amene anatiphera ambiri.

25. Ndipo kunali, pakukondwera mitima yao, anati, Kaitaneni Samsoni, atisewerere. Naitana Samsoni m'kaidi; nasewera iye pamaso pao; ndipo anamuika iye pakati pa mizati.

26. Ndipo Samsoni anati kwa mnyamata womgwira dzanja, Ndileke, ndikhudze mizati imene nyumba ikhazikikapo, kuti nditsamirepo.

27. Koma nyumbayi inadzala ndi amuna ndi akazi; ndi akalonga onse a Afilisti anali momwemo ndi patsindwi panali amuna ndi akazi ngati zikwi zitatu akuyang'ana pakusewera Samsoni.

28. Pamenepo Samsoni anaitana kwa Yehova, nati, Yehova, Mulungu, dikupempha mundikumbukile, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthawi yino yokha, Mulungu, kuti ndidzilipsiriretu tsopano apa Afilisti, cifukwa ca maso anga awiri.

29. Ndipo Samsoni anagwira mizati iwiri ya pakati imene nyumba inakhazikikapo, natsamirapo wina ndi dzanja lamanja, ndi unzace ndi dzanja lamanzere.

30. Nati Samsoni, Ndife nao Afilisti; nadziweramira mwamphamvu; ndipo nyumba idagwa pa akalonga, ndi pa anthu onse anali m'mwemo. Motero akufa amene anawapha pa kufa kwace anaposa amene anawapha akali moyo.

31. Pamenepo anatsika abale ace ndi banja lonse la atate wace, namnyamula, Dakwera naye, namuika pakati pa Zora ndi Esitaoli, m'manda a Manowa atate wace. Ndipo adaweruza Israyeli zaka makumi awiri.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 16