Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Oweruza 10:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Atafa Abimeleki, anauka kupulumutsa Israyeli Tola mwana wa Puwa, mwana wa Dodo munthu wa Isakara; nakhala iye m'Sanriri ku mapiri a Efraimu.

2. Ndipo anaweruza Israyeli zaka makumi awiri ndi zitatu, nafa, naikidwa m'Samiri.

3. Atafa iye, anauka Yairi Mgileadi, naweruza Israyeli zaka makumi awiri mphambu ziwiri.

4. Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu okwera pa ana a aburu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo midzi makumi atatu, ochedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Gileadi.

Werengani mutu wathunthu Oweruza 10