Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Obadiya 1:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Cifukwa ca ciwawa unamcitira mphwako Yakobo, udzakutidwa ndi manyazi, nudzaonongeka ku nthawi yonse.

11. Tsiku lija unaima padera, tsiku lija alendo anagwira ndende makamu ace, nalowa m'zipata zace acilendo, nacitira Yerusalemu maere, iwenso unakhala ngati mmodzi wa iwowa.

12. Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka cikhakha tsiku lakupsinjika.

13. Usalowe m'mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe coipa cao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao.

14. Ndipo usaime pamphambano kuononga opulumuka ace; kapena kupereka otsala ace tsiku lakupsinjika.

15. Pakuti tsiku la Yehova layandikira amitundu onse; monga unacita iwe, momwemo adzakucitira; cocita iwe cidzakubwererapamtupako.

16. Pakuti monga munamwa pa phiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo.

17. Koma m'phiri la Ziyoni mudzakhala opulumuka, ndipo lidzakhala lopatulika; ndi a nyumba ya Yakobo adzakhala nazo zolowa zao.

Werengani mutu wathunthu Obadiya 1