Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 6:9-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi;Ndiye wobadwa yekha wa amace;Ndiye wosankhika wa wombala.Ana akazi anamuona, namucha wodala;Ngakhale akazi akulu a mfumu, ndi akazi ang'ono namtamanda.

10. Nati, Ndaniyo aturuka ngati mbanda kuca,Wokongola ngati mwezi,Woyera ngati dzuwa,Woopsya ngati nkhondo ndi mbendera?

11. Ndinatsikira ku munda wa ntedza,Kukapenya msipu wa m'cigwa,Kukapenya ngati pamipesa paphuka,Ngati pamakangaza patuwa maluwa.

12. Ndisanazindikire, moyo wanga unandiimikaPakati pa magareta a anthu anga aufulu.

13. Anati, Bwera, bwera, Msulamiwe;Bwera, bwera, tiyang'ane pa iwe.Muyang'aniranji pa Msulami,Ngati pa masewero akuguba?

Werengani mutu wathunthu Nyimbo 6