Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 6:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Undipambutsire maso ako, Pakuti andiopetsa.Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi,Zigona pambali pa Gileadi.

6. Mano ako akunga gulu la nkhosa zazikazi,Zikwera kucokera kosamba; Yonse iri ndi ana awiri,Palibe imodzi yopoloza.

7. Palitsipa pako pakunga phande la khangazaPatseri pa cophimba cako.

8. Alipo akazi akulu a mfumu makumi asanu ndi limodzi,Kudza akazi ang'ono makumi asanu ndi atatu,Ndi anamwali osawerengeka.

9. Nkhunda yanga, wangwiro wangayu, ndiye mmodzi;Ndiye wobadwa yekha wa amace;Ndiye wosankhika wa wombala.Ana akazi anamuona, namucha wodala;Ngakhale akazi akulu a mfumu, ndi akazi ang'ono namtamanda.

Werengani mutu wathunthu Nyimbo 6