Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 2:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndine duwa lofiira la ku Saroni,Ngakhale kakombo wa kuzigwa.

2. Ngati kakombo pakati pa mingaMomwemo wokondedwa wanga pakati pa ana akazi.

3. Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango,Momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana amuna.Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wace,Zipatso zace zinatsekemera m'kamwa mwanga.

4. Anandifikitsa ku nyumba ya vinyo,Mbendera yace yondizolimira inali cikondi.

5. Mundilimbikitse ndi mphesa zouma, munditonthoze mtima ndi maula,Pakuti ndadwala ndi cikondi.

6. Dzanja lace lamanzere anditsamiritse kumutu,Dzanja lace lamanja ndi kundifungatira.

7. Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,Pali mphoyo, ndi nswala za kuthengo,Kuti musautse, ngakhale kugalamutsa cikondi,Mpaka cikafuna mwini.

8. Mau a wokondedwa wanga mnyamatayo! Taona, adza,Alikulumpha pamapiri, alikujidimuka pazitunda.

9. Wokondedwa wanga akunga mphoyo, pena mwana wa mbawala:Taona, aima patseri pa khoma pathu,Apenyera pazenera, Nasuzumira pamade.

Werengani mutu wathunthu Nyimbo 2