2. Ana a Israyeli acite Paskha pa nyengo yoikidwa.
3. Tsiku lakhumi ndi cinai la mweziwo, madzulo, muziucita, pa nyengo yace yoikidwa; muucite monga mwa malemba ace onse, ndi maweruzo ace onse.
4. Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli, kuti acite Paskha.
5. Ndipo anacita Paskha mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mweziwo, madzulo, m'cipululu ca Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israyeli anacita.
6. Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoza kucita Paskha tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;
7. nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere naco copereka ca Yehova pa nyengo yace yoikidwa, pakati pa ana a Israyeli?
8. Ndipo Mose ananena nao, Baimani; ndimve couza Yehova za inu.
9. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,