Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 9:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'cipululu ca Sinai, mwezi woyamba wa caka caciwiri ataturuka m'dziko la Aigupto, ndi kuti,

2. Ana a Israyeli acite Paskha pa nyengo yoikidwa.

3. Tsiku lakhumi ndi cinai la mweziwo, madzulo, muziucita, pa nyengo yace yoikidwa; muucite monga mwa malemba ace onse, ndi maweruzo ace onse.

4. Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli, kuti acite Paskha.

5. Ndipo anacita Paskha mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mweziwo, madzulo, m'cipululu ca Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israyeli anacita.

6. Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoza kucita Paskha tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;

7. nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere naco copereka ca Yehova pa nyengo yace yoikidwa, pakati pa ana a Israyeli?

8. Ndipo Mose ananena nao, Baimani; ndimve couza Yehova za inu.

9. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

Werengani mutu wathunthu Numeri 9