Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 7:9-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Koma sanapatsa ana a Kohati kanthu; popeza nchito yao ndiyo ya zinthu zopatulika, zimene amazisenza pa mapewa ao.

10. Ndipo akalonga anabwera nazo za kupereka ciperekere guwa la nsembe tsiku lodzozedwa ili; inde akalongawo anabwera naco copereka cao pa guwa la nsembelo.

11. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Akalonga onse, yense pa tsiku lace, apereke zopereka zao za kupereka ciperekere guwa la nsembe.

12. Wakubwera naco copereka cace tsiku loyamba ndiye Nahesoni mwana wa Aminadabu, wa pfuko la Yuda:

13. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace ndiko masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwirizo zodzala ndi ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta ukhale nsembeyaufa;

14. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

15. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

16. ronde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

17. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa: asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Nahesoni mwana wa Aminadabu.

18. Tsiku laciwiri Netaneli mwana wa Zuwara, kalonga wa Isakara, anabwera naco cace:

19. anabwera naco copereka cace mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

20. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

21. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

22. tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo;

23. ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, ana a nkhosa asanu a caka cimodzi; ndico copereka ca Netaneli mwana wa Zuwara.

24. Tsiku lacitatu kalonga wa ana a Zebuloni, ndiye Eliyabu mwana wa Heloni:

25. copereka cace ndico mbizi imodzi yasiliva, kulemera kwace masekeli zana limodzi ndi makumi atatu, mbale yowazira imodzi yasiliva ya masekeli makumi asanu ndi awiri, kuyesa sekeli wa malo opatulika; zonse ziwiri zodzala ndi ufa wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa;

26. cipande cimodzi cagolidi ca masekeli khumi, codzala ndi cofukiza;

27. ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwana wa nkhosa mmodzi wa caka cimodzi, zikhale nsembe yopsereza;

Werengani mutu wathunthu Numeri 7