1. Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kumuutsa kacisi, namdzoza ndi kumpatula, ndi zipangizo zace zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zace zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;
2. akalonga a Israyeli, akuru a nyumba za makolo ao, anapereka nsembe, ndiwo akalonga a mapfuko akuyang'anira owerengedwa;
3. anadza naco copereka cao pamaso pa Yehova, magareta ophimbika asanu ndi mmodzi, ndi ng'ombe khumi ndi ziwfri; akalonga awiri anapereka gareta mmodzi, ndi kalonga mmodzi ng'ombe imodzi; nabwera nazo pakhomo pa kacisi.
4. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
5. Uzilandira kwa iwo, kuti zikhale zakucitira nchito ya cihema cokomanako; nuzipereke kwa Alevi, yense monga mwa nchito yace.
6. Ndipo Mose analandira magareta ndi ng'ombe, nazipereka kwa Alevi.
7. Anapatsa ana a Gerisoni magareta awiri ndi ng'ombe zinai, monga mwa nchito yao;
8. napatsa ana a Merari magareta anai ndi ng'ombe zisanu ndi zitatu, monga mwa nchito yao; wakuziyang'anira ndiye Itamara mwana wa Aroni wansembe.
9. Koma sanapatsa ana a Kohati kanthu; popeza nchito yao ndiyo ya zinthu zopatulika, zimene amazisenza pa mapewa ao.
10. Ndipo akalonga anabwera nazo za kupereka ciperekere guwa la nsembe tsiku lodzozedwa ili; inde akalongawo anabwera naco copereka cao pa guwa la nsembelo.