Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 5:26-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, cikumbutso cace, nacitenthe pa guwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo.

27. Ndipo atammwetsa madziwo, kudzatero, ngati wadetsedwa, nacita mosakhulupitika pa mwamuna wace, madzi odzetsa tembererowo adzalowa mwa iye nadzamwawira, nadzamtupitsa mbulu, ndi m'cuuno mwace mudzaonda; ndi mkaziyo adzakhala temberero pakati pa anthu a mtundu wace.

28. Koma ngati mkazi sanadetsedwa, nakhala woyera, pamenepo adzapulumuka, nadzaima.

29. Ici ndi cilamulo ca nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wace, ampatukira nadetsedwa;

30. kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo acitira mkazi wace nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amcitire cilamulo ici conse.

31. Mwamunayo ndiye wosacita mphulupulu, koma mkazi uyo asenze mphulupulu yace.

Werengani mutu wathunthu Numeri 5