Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 5:23-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.

24. Ndipo amwetse mkaziyo madzi owawa akudzetsa temberero; ndi madzi odzetsa temberero adzalowa mwa iye nadzamwawira.

25. Ndipo wansembe atenge nsembe yaufa m'manja mwa mkazi, naweyule nsembe yaufa pamaso pa Yehova, nabwere nayo ku guwa la nsembe.

26. Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, cikumbutso cace, nacitenthe pa guwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo.

27. Ndipo atammwetsa madziwo, kudzatero, ngati wadetsedwa, nacita mosakhulupitika pa mwamuna wace, madzi odzetsa tembererowo adzalowa mwa iye nadzamwawira, nadzamtupitsa mbulu, ndi m'cuuno mwace mudzaonda; ndi mkaziyo adzakhala temberero pakati pa anthu a mtundu wace.

28. Koma ngati mkazi sanadetsedwa, nakhala woyera, pamenepo adzapulumuka, nadzaima.

29. Ici ndi cilamulo ca nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wace, ampatukira nadetsedwa;

30. kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo acitira mkazi wace nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amcitire cilamulo ici conse.

31. Mwamunayo ndiye wosacita mphulupulu, koma mkazi uyo asenze mphulupulu yace.

Werengani mutu wathunthu Numeri 5