Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 4:37-49 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. Awa ndi owerengedwa a mabanja a Akohati, onse akutumikira m'cihema cokomanako, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.

38. Ndipo ana owerengedwa a Gerisoni, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyu mba za makolo ao,

39. kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu, kuti agwire nchito m'cihema cokomanako,

40. owerengedwa ao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi kudza makumi atatu.

41. Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Gerisoni, onse akutumikira m'cihema cokomanako, adawawerenga Mose ndi Aroni monga mwa mau a Yehova.

42. Ndipo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao,

43. kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa utumikiwu kuti agwire nchito m'cihema cokomanako,

44. owerengedwa ao monga mwa mabanja ao, ndiwo zikwi zitatu ndi mazana awiri.

45. Amenewo ndiwo owerengedwa a mabanja a ana a Merari, amene Mose ndi Aroni anawawerenga monga mwa mau a Yehova mwa dzanja la Mose.

46. Owerengedwa onse a Alevi, amene Mose ndi Aroni ndi akalonga a Israyeli anawawerengera, monga mwa mabanja ao, ndi monga mwa nyumba za makolo ao,

47. kuyambira a zaka makumi atatu ndi mphambu kufikira a zaka makumi asanu, onse akulowa kugwira nchito ya utumikiwu, ndiyo nchito ya akatundu m'cihema cokomanako;

48. owerengedwa ao ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu mphambu makumi asanu ndi atatu.

49. Anawawerenga monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose, onse monga mwa nchito zao, ndi monga mwa akatundu ao; anawawerenga monga momwe Yehova adauza Mose.

Werengani mutu wathunthu Numeri 4