Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 35:28-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. popeza wakupha munthu akadakhala m'mudzi wace wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lace lace.

29. Ndipo izi zikhale kwa inu lemba la ciweruzo mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zonse.

30. Ali yense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe.

31. Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, naparamula imfa; koma aziphedwa ndithu.

32. Musamalandira dipo lakuombola iye amene adathawira ku mudzi wace wopulumukirako, kuti abwerenso kukhala m'dziko, kufikira atafa wansembe.

33. Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko cifukwa ca mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.

34. Usamadetsa dziko ukhala m'mwemo, limene ndikhalitsa pakati pace; popeza Ine Yehova ndikhalitsa pakati pa ana a Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Numeri 35