Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 35:19-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Wolipsa mwazi mwini wace aphe wakupha munthuyo; pakumkumika amuphe,

20. Ndipo akampyoza momkwiyira, kapena kumponyera kanthu momlalira, kuti wafa;

21. kapena kumpanda ndi dzanja lace momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo pomkumika.

22. Koma akampyoza modzidzimuka, osamuda, kapena kumponyera kanthu osamialira,

23. kapena kumponyera mwala wakufetsa munthu, osamuona, namgwetsera uwu, kuti wafa, koma sindiye mdani wace, kapena womfunira coipa;

24. pamenepo msonkhano uziweruza pakati pa wokantha mnzaceyo ndi wolipsa mwaziyo monga mwa maweruzo awa;

25. ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m'dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere ku mudzi wace wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.

26. Koma wakupha munthu akaturuka nthawi iri yonse kulumpha malire a mudzi wace wopulumukirako kumene anathawirako;

27. nakampeza wolipsa mwazi kunja kwa malire a mudzi wace wothawirako, ndipo wolipsa mwazi akapha wakupha munthu, alibe kucimwira mwazi;

28. popeza wakupha munthu akadakhala m'mudzi wace wopulumukirako kufikira atafa mkulu wa ansembe; koma atafa mkulu wa ansembe wakupha munthuyo abwere ku dziko lace lace.

29. Ndipo izi zikhale kwa inu lemba la ciweruzo mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zonse.

30. Ali yense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe.

31. Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, naparamula imfa; koma aziphedwa ndithu.

32. Musamalandira dipo lakuombola iye amene adathawira ku mudzi wace wopulumukirako, kuti abwerenso kukhala m'dziko, kufikira atafa wansembe.

33. Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko cifukwa ca mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.

34. Usamadetsa dziko ukhala m'mwemo, limene ndikhalitsa pakati pace; popeza Ine Yehova ndikhalitsa pakati pa ana a Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Numeri 35