Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 33:51-56 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

51. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Mutaoloka Yordano kulowa m'dziko la Kanani,

52. mupitikitse onse okhala m'dzikopamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse;

53. ndipo mulande dziko, ndi kukhala m'mwemo, pakuti ndinakupatsani inu dzikoli likhale lanu lanu.

54. Ndipo mulandire dzikoli ndi kucita maere monga mwa mabanja anu; colowa cao cicurukire ocurukawo, colowa cao cicepere ocepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwace; mulandire colowa canu monga mwa mapfuko a makolo anu.

55. Koma mukapanda kupitikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakubvutani m'dziko limene mukhalamo.

56. Ndipo kudzakhala kuti monga ndinayesa kucitira iwowa, ndidzakucitirani inu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 33