Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 33:24-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Nacokera ku phiri la Saferi, nayenda namanga n'Harada.

25. Nacokera ku Harada, nayenda namanga m'Makeloti.

26. Nacokera ku Makeloti, nayenda namanga m'Tahata.

27. Nacokera ku Tahata, nayenda namanga m'Tara.

28. Nacokera ku Tara, nayenda namanga m'Mitika.

29. Nacokera ku Mitika, nayenda namanga m'Hasimona.

30. Nacokera ku Hasimona, nayenda namanga m'Moseroto.

31. Nacokera ku Moseroto, nayenda namanga m'Bene Yaakana.

32. Nacokera ku Bene Yaakana, nayenda namanga m'Hori Hagidigadi.

33. Nacokera ku Hori Hagidigadi, nayenda namanga m'Yotibata.

34. Nacokera ku Yotibata, nayenda namanga m'Abirona.

35. Nacokera ku Abirona, nayenda namanga m'Ezioni Geberi.

36. Nacokera ku Ezioni Geberi, nayenda namanga m'cipululu ca Zini (ndiko Kadesi).

37. Nacokera ku Kadesi, nayenda namanga m'phiri la Hori, ku malekezero a dziko la Edomu.

38. Ndipo Aroni wansembe anakwera m'phiri la Hori pa mau a Yehova, nafa komweko, ataturuka ana a Israyeli m'dziko la Aigupto zaka makumi anai, mwezi wacisanu, tsiku loyamba la mwezi.

39. Ndipo Aroni ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi awiri kudza zitatu pakufa iye m'phiri la Hori.

40. Ndipo Mkanani, mfumu ya Aradi, wakukhala kumwela m'dziko la Kanani, anamva za kudza kwao kwa ana a Israyeli.

41. Ndipo anacokera ku phiri la Hori, nayenda namanga m'Tsalimona.

42. Nacokera ku Tsalimona, nayenda namanga m'Punoni.

Werengani mutu wathunthu Numeri 33