Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 33:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo Mose analembera maturukidwe ao monga mwa maulendo ao, monga mwa mau a Yehova; ndipo maulendo ao ndi awa monga mwa maturukidwe ao.

3. Ndipo anacokera ku Ramese mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi woyamba; atacita Paskha m'mawa mwace ana a Israyeli, anaturuka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aaigupto onse,

4. pamene Aaigupto ailalikuika oyamba kubadwa ao onse, amene Yehova adawakantha; Yehova adaweruzanso milungu yao.

5. Ndipo ana a Israyeli macokera ku Ramese, nayenda namanga ku Sukoti.

6. Nacokera ku Sukoti, nayenda namanga m'Etamu, ndiko ku malekezero a cipululu.

7. Ndipo anacokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwace kwa Baala Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli.

8. Ndipo anacokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'cipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'cipululu ca Etamu, namanga m'Mara.

9. Ndipo anacokera ku Mara, nayenda nafika ku Elimu, ku Elimu ndiko kuli akasupe khumi ndi awiri a madzi, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; namanga iwo komweko.

10. Ndipo anacokera ku Elimu, nayenda namanga ku Nyanja Yofiira.

11. Nacokera ku Nyanja Yofiira, nayenda namanga m'cipululu ca Sini.

12. Nacokera ku cipululu ca Sini, nayenda namanga m'Dofika.

13. Nacokera ku Dofika, nayenda namanga m'Alusi.

14. Nacokera ku Alusi, nayenda namanga m'Refidimu; kumeneko kunalibe madzi kuti anthu amwe.

Werengani mutu wathunthu Numeri 33