Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 33:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Maulendo a ana a Israyeli amene anaturuka m'dziko la Aigupto monga mwa makamu ao, ndi dzanja la Mose ndi Aroni, ndi awa.

2. Ndipo Mose analembera maturukidwe ao monga mwa maulendo ao, monga mwa mau a Yehova; ndipo maulendo ao ndi awa monga mwa maturukidwe ao.

3. Ndipo anacokera ku Ramese mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi woyamba; atacita Paskha m'mawa mwace ana a Israyeli, anaturuka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aaigupto onse,

4. pamene Aaigupto ailalikuika oyamba kubadwa ao onse, amene Yehova adawakantha; Yehova adaweruzanso milungu yao.

5. Ndipo ana a Israyeli macokera ku Ramese, nayenda namanga ku Sukoti.

6. Nacokera ku Sukoti, nayenda namanga m'Etamu, ndiko ku malekezero a cipululu.

7. Ndipo anacokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwace kwa Baala Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli.

8. Ndipo anacokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'cipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'cipululu ca Etamu, namanga m'Mara.

Werengani mutu wathunthu Numeri 33