Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 32:20-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo Mose anati nao, Ngati mudzacita ici, ndi kudzikonza kunkhondo pamaso pa Yehova,

21. ndi kuoloka Yordano pamaso pa Yehova okonzeka onse mwa inu, kufikira atapitikitsa adani ace pamaso pace,

22. ndi dziko lagonjera Yehova; mutatero mudzabwerere, ndi kukhala osacimwira Yehova ndi Israyeli; ndipo dziko ili lidzakhala lanu lanu pamaso pa Yehova.

23. Koma mukapanda kutero, taonani, mwacimwira Yehova; ndipo zindikirani kuti cimo lanu lidzakupezani.

24. Dzimangireni midzi ya ana anu, ndi makola a zoweta zanu; ndipo muzicite zoturuka m'kamwa mwanu.

25. Ndipo ana a Gadi ndi ana a Rubeni ananena ndi Mose, nati, Anyamata anu adzacita monga mbuyanga alamulira.

26. Ana athu, akazi athu, zoweta zathu, ndi ng'ombe zathu zonse, zidzakhala komweko m'midzi ya ku Gileadi;

27. koma anyamata anu adzaoloka, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova kunkhondo, monga wanena mbuyanga.

28. Pamenepo Mose anamuuza Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akuru a makolo a mapfuko a ana a Israyeli za iwo.

29. Ndipo Mose anati kwa iwo, Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni aoloka nanu Yordano, yense wokonzekera ndi zankhondo pamaso pa Yehova, ndi dziko lagonjera inu; pamenepo muwapatse dziko la Gileadi likhale lao lao;

30. koma akapanda kuoloka nanu okonzeka, akhale nao maiko ao ao pakati pa inu m'dziko la Kanani.

Werengani mutu wathunthu Numeri 32