Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 31:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2. Abwezereni cilango Amidyani cifukwa ca ana a Israyeli; utatero udzaitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wako.

3. Ndipo Mose ananena ndi anthu, nati, Adzikonzere ena mwa inu zida za nkhondo, alimbane nao Amidyani, kuwabwezera Amidyani cilango ca Yehova.

4. Muwatume kunkhondo a pfuko limodzi, cikwi cimodzi, a pfuko limodzi cikwi cimodzi, atere mafuko onse a Israyeli.

5. Ndipo anapereka mwa zikwi za Israyeli, a pfuko limodzi cikwi cimodzi, anthu zikwi khumi ndi ziwiri okonzekeratu ndi zankhondo.

6. Ndipo Mose anawatuma a pfuko limodzi cikwi cimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Pinehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lace.

7. Ndipo anawathira nkhondo Amidyani, monga Yehova adamuuza Mose; nawapha amuna onse.

8. Ndipo anapha mafumu a Amidyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekamu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.

9. Ndipo ana a Israyeli anagwira akazi a Amidyani, ndi ana ang'ono, nafunkha ng'ombe zao zonse, ndi zoweta zao zonse, ndi cuma cao conse.

Werengani mutu wathunthu Numeri 31