Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 3:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo azisunga udikiro wace, ndi udikiro wa khamu lonse pa khomo la cihema cokomanako, kucita nchito ya kacisi.

8. Ndipo asunge zipangizo zonse za cihema cokomanako, ndi udikiro wa ana a Israyeli, kuicita nchito ya kacisi.

9. Ndipo uzipereka Alevi kwa Aroni ndi kwa ana ace amuna; apatsidwa kwa iye ndithu, ocokera kwa ana a Israyeli.

10. Koma uike Aroni ndi ana ace amuna, azisunga nchito yao ya nsembe; ndi mlendo wakusendera pafupi amuphe.

11. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

12. Ndipo taonani, Ine ndatenga Alevi kuwacotsa pakati pa ana a Israyeli m'malo mwa ana ovamba onse, oyamba kubadwa mwa ana a Israyeli; ndipo Aleviwo ndi anga.

13. Pakuti ana oyamba onse ndi anga; tsiku lija ndinakantha ana oyamba onse m'dziko la Aigupto ndinadzipatulira ana oyamba onse m'Israyeli, kuyambira munthu kufikira coweta; ndiwo anga; Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Numeri 3