Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 3:26-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. ndi nsaru zocinga za kubwalo, ndi nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo, lokhala kukacisi, ndi ku guwa la nsembe pozungulira, ndi zingwe zace za ku nchito zace zonse.

27. Banja la Aamiramu, ndi banja la Aizara, ndi banja la Ahebroni, ndi banja la Auziyeli ndiwo a Kohati; ndiwo mabanja a Akohati.

28. Powawerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi, akusunga udikiro wa pa malo opatulika.

29. Mabanja a ana a Kohati azimanga mahema ao pa mbali ya kacisi ya kumwera.

30. Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo ao ya mabanja a Akohati ndiye Elizafana mwana wa Uziyeli.

31. Ndipoudikirowaondiwo likasa, ndi gome, ndi coikapo nyali, ndimagome a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene acita nazo, ndi nsaru yocinga, ndi nchito zace zonse.

32. Ndipo kalonga wa akalonga a Alevi ndiye Eleazara mwana wa Aroni wansembeyo; ndiye aziyang'anira osunga udikiro wa pa malo opatulika.

33. Banja la Amali, ndi banja la Amusi ndiwo a Merari; ndiwo mabanja a Merari.

34. Ndipo owerengedwa ao, powerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi zisanu ndi cimodzi kudza mazana awiri.

35. Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja a Merari ndiye Zuriyeli mwana wa Abiyaili; azimanga mahema ao pa mbali ya kacisi ya kumpoto.

Werengani mutu wathunthu Numeri 3