Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 29:26-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndi tsiku lacisanu ng'ombe zisanu ndi zinai, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, opanda cirema;

27. ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;

28. ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

29. Ndi tsiku lacisanu ndi cimodzi ng'ombe zisanu ndi zitatu, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, opanda cirema;

30. ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;

31. ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

32. Ndi tsiku lacisanu ndi ciwiri ng'ombe zisanu ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai, a caka cimodzi, opanda cirema;

33. ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa yamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;

34. ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

35. Tsiku lacisanu ndi citatu muzikhala nalo tsiku loletsa; musamacita nchito ya masiku ena;

36. koma mubwere nayo nsembe yopsereza ndiyo nsembe yamoto, ya pfungo lokoma kwa Yehova: ng'ombe imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, ana a nkhosa asanu ndi awiri, a caka cimodzi, opanda cirema;

37. nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;

38. ndi tonde mmodzi wa nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

39. Izi muzikonzera Yehova mu nyengo zanu zoikika, pamodzi ndi zowinda zanu, ndi zopereka zanu zaufuru, za nsembe zanu zopsereza, ndi za nsembe zanu zaufa, ndi za nsembe zanu zothira, ndi za nsembe zanu zoyamika.

40. Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose.

Werengani mutu wathunthu Numeri 29