Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 29:14-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. ndi nsembe yace yaufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe imodzi, momwemo nazo ng'ombe khumi ndi zitatuzo, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, momwemo nazo nkhosa zamphongo ziwirizo;

15. ndi limodzi la magawo khumi likhale la mwana wa nkhosa mmodzi, momwemo nao ana a nkhosa khumi ndi anai;

16. ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, nsembe yace yaufa, ndi nsembe yace yothira.

17. Ndipo tsiku laciwiri muzibwera nazo ng'ombe zamphongo khumi ndi ziwiri, nkhosa zamphongo ziwiri, ana a nkhosa khumi ndi anai a caka cimodzi, opanda cirema;

18. ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira, za ng'ombe, za nkhosa zamphongo, ndi za ana a nkhosa, monga mwa kuwerenga kwace, ndi kutsata lemba lace;

19. ndi tonde mmodzi akhale nsembe yaucimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yace yaufa, ndi nsembe zace zothira.

Werengani mutu wathunthu Numeri 29